Album Cover Nsokoto

Nsokoto

The Very Best

5

Kumsokoto kuli mfiti imodzi inkalodza ana osalakwa

Kupata kwa ana iyo sinkasangalatsidwa nako

Mwana apate eti tiona ngati agone

Chaka chino chokha iye akagonera kumanda

M'mati n'kwere ndakwera panyumba yanthakati

Wakoma bana pawaka

Wamara bana nsokoto

Mwana akangoti agone

Kum'bwerera usiku

Thupi lonse lamangika

Kulephera kufuula

Poti adsuke mam'mawa

Thupi kunjenjemera

Mutu wanga, malungo, matenda aja akula

Wakoma bana

Wati kitasha

Wamara bana

Ichi n'chasoni

Nsokoto nsokoto

Nsokoto nsokoto

Muuze nthakatiyo namulondola ife takana

Bana bakunsokoto ise

Bana bakumulowe ise

Bana bamwakisulu ise

Bana bakaronga ise

Bana bakurumphi ise

Bana bakuchitipa ise